Petro Achiritsa Wolumala Miyendo

1Tsiku lina Petro ndi Yohane ankapita ku Nyumba ya Mulungu kukapemphera nthawi ya 3 koloko masana. 2Ndipo munthu wolumala chibadwire ankanyamulidwa tsiku ndi tsiku kukayikidwa pa khomo la Nyumbayo lotchedwa Khomo Lokongola kuti azikapempha amene amalowa ku bwalo la Nyumbayo. 3Ataona Petro ndi Yohane ali pafupi kulowa anawapempha ndalama. 4Iwo anamuyangʼanitsitsa iye. Kenaka Petro anati, “Tiyangʼane!” 5Munthuyo anawayangʼanitsitsa kuyembekezera kuti alandira kanthu kuchokera kwa iwo.

6Petro anati kwa iye, “Ine ndilibe siliva kapena golide, koma chimene ndili nacho ndikupatsa. Mʼdzina la Yesu Khristu wa ku Nazareti, yenda.” 7Ndipo anamugwira dzanja lamanja, namuthandiza kuti ayimirire ndipo nthawi yomweyo mapazi ake ndi akakolo ake analimba. 8Iye analumpha ndi kuyamba kuyenda. Kenaka analowa nawo pamodzi mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu, akuyenda ndi kulumpha ndiponso kuyamika Mulungu. 9Anthu onse atamuona akuyenda ndiponso kuyamika Mulungu, 10anamuzindikira kuti ndi yemwe uja ankakhala pa khomo la Nyumbayo lotchedwa Khomo Lokongola, ndipo anazizwa ndi kudabwa ndi zimene zinamuchitikira.