Efodi

6“Apange efodi pogwiritsa ntchito golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira yolukidwa mwaluso. 7Efodiyo ikhale ndi timalamba tiwiri ta pa mapewa tosokerera ku msonga zake ziwiri kuti azitha kumanga. 8Lamba womangira efodi akhale wolukidwa mwaluso ngati efodiyo. Akhale wopangidwa ndi golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yofewa yosalala.

9“Utenge miyala iwiri ya onikisi ndipo uzokotepo mayina a ana a Israeli. 10Mayina asanu ndi limodzi akhale pa mwala umodzi, ndipo mayina asanu ndi limodzi pa mwala winawo motsata mabadwidwe awo. 11Mayina a ana a Israeli uwazokote pa miyala iwiriyo, monga momwe amachitira mmisiri wozokota miyala. Ndipo uyike miyalayo mu zoyikamo zake zagolide. 12Umangirire miyala iwiriyi pa tinsalu ta mʼmapewa ta efodi tija ngati miyala ya chikumbutso cha ana a Israeli. Aaroni azinyamula mayinawo mʼmapewa ake kuti akhale chikumbutso pamaso pa Yehova. 13Upange zoyikamo za maluwa agolide, 14ndiponso maunyolo awiri a golide wabwino kwambiri, wopetedwa ngati zingwe ndipo uwalumikize ku zoyikamozo.