Ayuda Apitirira Kusakhulupirira

37Ngakhale Yesu anachita zizindikiro zodabwitsa zonsezi pamaso pawo, sanamukhulupirirebe. 38Izi zinakwaniritsa mawu a mneneri Yesaya kuti:

“Ambuye, wakhulupirira uthenga wathu ndani,

ndipo ndi kwa yani komwe mkono wa Ambuye wavumbulutsidwa?”

39Pa chifukwa cha ichi iwo sanakhulupirire, chifukwa Yesaya ananenanso kuti:

40“Iye wachititsa khungu maso awo

ndi kuwumitsa mitima yawo,

kotero kuti iwo sangathe kuona ndi maso awo,

kapena kuzindikira ndi mitima yawo,

kapena kutembenuka kuti Ine ndikanawachiza.”

41Yesaya ananena izi chifukwa anaona ulemerero wa Yesu ndi kuyankhula za Iye.

42Komabe pa nthawi yomweyi ambiri ngakhale atsogoleri anakhulupirira Iye. Koma chifukwa cha Afarisi iwo sanavomereze chikhulupiriro chawo chifukwa amaopa kuti angawatulutse mʼsunagoge; 43pakuti iwo amakonda kuyamikiridwa ndi anthu kuposa kuyamikiridwa ndi Mulungu.

44Kenaka Yesu anafuwula nati, “Munthu aliyense amene akhulupirira Ine, sakhulupirira Ine ndekha, komanso Iye amene anandituma Ine. 45Iye amene waona Ine, waonanso Iye amene anandituma Ine. 46Ine ndabwera mʼdziko lapansi monga kuwunika, kotero palibe amene amakhulupirira Ine nʼkumakhalabe mu mdima.

47“Ndipo munthu amene amva mawu anga koma osawasunga, Ine sindimuweruza. Pakuti Ine sindinabwere kudzaweruza dziko lapansi, koma kudzapulumutsa. 48Iye amene akana Ine ndipo salandira mawu anga ali ndi womuweruza. Tsiku lomaliza mawu amene ndiyankhulawa adzamutsutsa. 49Pakuti Ine sindiyankhula mwa Ine ndekha, koma Atate amene anandituma amandilamulira choti ndinene ndi momwe ndinenere. 50Ine ndikudziwa kuti lamulo lake ndi moyo wosatha. Choncho chilichonse chimene Ine ndinena ndi chimene Atate andiwuza.”