Yesu Asandutsa Madzi Kukhala Vinyo
1Pa tsiku lachitatu munali ukwati mu Kana wa ku Galileya. Amayi ake a Yesu anali komweko, 2ndipo Yesu ndi ophunzira ake anayitanidwanso ku ukwatiwo. 3Vinyo atatha, amayi a Yesu anati kwa Iye, “Wawathera vinyo.”
4Yesu anayankha kuti, “Amayi, chifukwa chiyani mukundiwuza Ine? Nthawi yanga sinakwane.”
5Amayi ake anati kwa antchito, “Inu muchite chilichonse chimene akuwuzeni.”
6Pamenepo panali mitsuko yamiyala yothiramo madzi isanu ndi umodzi, imene Ayuda amagwiritsa ntchito pa mwambo wodziyeretsa. Uliwonse unali ndi malita 100 kapena kupitirirapo.
7Yesu anati kwa antchitowo, “Dzazani madzi mʼmitsukoyi,” ndipo iwo anadzaza ndendende.
8Ndipo Iye anatinso kwa iwo, “Tsopano tungani ndipo kaperekeni kwa mkulu waphwando.”
Iwo anachita momwemo. 9Mkulu waphwando analawa madziwo amene anasandulika vinyo, ndipo sanazindikire kumene vinyoyo anachokera, ngakhale kuti antchito amene anatunga madziwo amadziwa. Kenaka anayitanira mkwati pambali 10ndipo anati, “Aliyense amatulutsa vinyo wokoma kwambiri poyambirira ndipo kenaka vinyo wosakoma pamene oyitanidwa atamwa kale wambiri; koma iwe wasunga wokoma mpaka tsopano.”
11Ichi chinali chizindikiro chodabwitsa choyamba chimene Yesu anachita ku Kana wa ku Galileya. Potero Iye anawulula ulemerero wake, ndipo ophunzira ake anamukhulupirira Iye.


