17Davide anapita kukakumana nawo ndipo anati, “Ngati mwabwera kwa ine mwamtendere, kuti mundithandize, ndakonzeka kugwirizana nanu. Koma ngati mwabwera kudzandipereka kwa adani anga, ngakhale kuti sindinalakwe, Mulungu wa makolo anthu aone izi ndipo akuweruzeni.”