10anatumiza mwana wake Hadoramu kwa mfumu Davide kukamulonjera ndi kukamuyamikira chifukwa cha kupambana kwake pa nkhondo yake ndi Hadadezeriyo, amene analinso pa nkhondo ndi Tou. Hadoramu anabweretsa ziwiya zosiyanasiyana zagolide, zasiliva ndi zamkuwa.